344 | GEN 14:7 | Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara. |
1413 | GEN 46:26 | Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66. |
3806 | NUM 5:13 | nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita), |
4087 | NUM 13:11 | kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi; |
4994 | DEU 3:17 | Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga. |
5054 | DEU 4:48 | Dziko ili linayambira ku Aroeri cha kumphepete kwa khwawa la Arinoni ku phiri la Siyoni (limeneli ndi phiri la Herimoni), |
5276 | DEU 13:3 | chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), |
5281 | DEU 13:8 | milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi), |
5287 | DEU 13:14 | kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe), |
5316 | DEU 14:24 | Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri), |
5321 | DEU 14:29 | kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse. |
6040 | JOS 9:1 | Mafumu onse okhala kumadzulo kwa Yorodani atamva zimenezi pamodzi ndi mafumu okhala ku mayiko a ku mapiri, mu zigwa, mʼmbali mwa Nyanja yayikulu mpaka ku Lebanoni (mafumu a Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi), |
6309 | JOS 18:14 | Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo. |
6325 | JOS 19:2 | Dzikolo linaphatikiza zigawo izi: Beeriseba (ndi Seba), Molada, |
6396 | JOS 21:13 | Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina, |
9027 | 1KI 8:39 | pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo chitanipo kanthu. Muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita, popeza inu mumadziwa mtima wake (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu onse), |
9573 | 2KI 2:18 | Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?” |
9830 | 2KI 10:33 | kuyambira kummawa kwa Yorodani, dziko lonse la Giliyadi (chigawo cha Gadi, Rubeni ndi Manase), kuchokera ku Aroeri pafupi ndi chigwa cha Arinoni kudutsa Giliyadi mpaka ku Basani. |
10468 | 1CH 5:36 | Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu), |
10515 | 1CH 6:42 | Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa, |
11092 | 1CH 26:10 | Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri), |
11317 | 2CH 6:30 | pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita popeza Inu mumadziwa mtima wake, (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu), |
19895 | JER 35:3 | Choncho ndinakatenga Yaazaniya (mwana wa Yeremiya winanso amene anali mwana wa Habaziniya), abale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu. |
21611 | EZK 41:16 | mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), |
22058 | DAN 9:1 | Mʼchaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero (wochokera kwa Amedi), amene anakhala mfumu ya ku Babuloni, |
22501 | AMO 5:9 | Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa), |
24543 | MRK 7:11 | Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), |
24703 | MRK 10:46 | Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. |
25032 | LUK 1:70 | (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera), |
25229 | LUK 6:14 | Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu, |
26151 | JHN 1:38 | Atatembenuka, Yesu anaona iwo akumutsatira ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” Iwo anati, “Rabi (kutanthauza kuti Aphunzitsi), kodi mukukhala kuti?” |
26327 | JHN 6:1 | Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), |
26419 | JHN 7:22 | Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata. |
26960 | JHN 20:24 | Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. |
26969 | JHN 21:2 | Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. |
27432 | ACT 13:1 | Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. |
27439 | ACT 13:8 | Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. |
28600 | 1CO 8:5 | Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri), |
29654 | 1TH 2:17 | Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni. |