10 | GEN 1:10 | Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
12802 | EST 6:5 | Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.” “Mulowetseni,” Mfumu inalamulira. |
14091 | PSA 13:5 | mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa. |
17078 | PRO 21:24 | Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri. |
17405 | ECC 2:2 | “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” |
18928 | ISA 62:4 | Sadzakutchanso “Wosiyidwa,” ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.” Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.” Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.” Chifukwa Yehova akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako. |
22529 | AMO 6:10 | Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.” |
24868 | MRK 14:45 | Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. |
25344 | LUK 8:30 | Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. |
26860 | JHN 18:6 | Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi. |
28343 | ROM 13:9 | Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” |
30433 | JAS 5:12 | Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa. |
30861 | REV 5:14 | Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza. |
31008 | REV 14:13 | Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.” “Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.” |