89 | GEN 4:9 | Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” |
1119 | GEN 37:35 | Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake. |
2065 | EXO 20:13 | “Usaphe. |
2067 | EXO 20:15 | “Usabe. |
4410 | NUM 22:34 | Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.” |
5072 | DEU 5:17 | “Usaphe. |
5074 | DEU 5:19 | “Usabe. |
6695 | JDG 6:39 | Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” |
7958 | 1SA 28:13 | Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.” |
8097 | 2SA 3:13 | Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.” |
8762 | 1KI 1:42 | Iye akuyankhula, Yonatani mwana wa wansembe Abiatara anafika. Adoniya anati, “Lowa. Munthu wabwino ngati iwe ayenera kubweretsa nkhani yabwino.” |
8791 | 1KI 2:18 | Batiseba anayankha kuti, “Chabwino. Ndidzakuyankhulira kwa mfumu.” |
9352 | 1KI 18:8 | Eliya anayankha kuti, “Inde. Pita kawuze mbuye wako kuti, ‘Eliya wabwera.’ ” |
9410 | 1KI 19:20 | Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, “Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani.” Eliya anayankha kuti, “Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?” |
9700 | 2KI 6:22 | Elisa anayankha kuti, “Musawaphe. Kodi mungaphe anthu amene munawagwira pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa kenaka apite kwa mbuye wawo.” |
11994 | 2CH 35:23 | Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.” |
12378 | NEH 4:8 | Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” |
17847 | ISA 6:8 | Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?” Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!” |
19960 | JER 37:17 | Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?” Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.” |
20417 | LAM 2:16 | Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.” |
23911 | MAT 21:16 | Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?” Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti, “Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda mwatuluka mayamiko?” |
24948 | MRK 16:6 | Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. |
26275 | JHN 4:50 | Yesu anayankha kuti, “Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. |
26656 | JHN 12:7 | Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. |
31128 | REV 21:6 | Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. |