104 | GEN 4:24 | Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.” |
141 | GEN 6:3 | Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” |
935 | GEN 32:7 | Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.” |
24400 | MRK 4:8 | Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.” |