14 | GEN 1:14 | Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; |
16 | GEN 1:16 | Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. |
27 | GEN 1:27 | Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi. |
39 | GEN 2:8 | Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. |
41 | GEN 2:10 | Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi. |
42 | GEN 2:11 | Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
47 | GEN 2:16 | Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu; |
50 | GEN 2:19 | Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. |
52 | GEN 2:21 | Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
54 | GEN 2:23 | Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.” |
66 | GEN 3:10 | Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.” |
71 | GEN 3:15 | Ndipo ndidzayika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; Iye adzaphwanya mutu wako ndipo iwe udzaluma chidendene chake.” |
72 | GEN 3:16 | Kwa mkaziyo Iye anati, “Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.” |
75 | GEN 3:19 | Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.” |
87 | GEN 4:7 | Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” |
92 | GEN 4:12 | Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.” |
94 | GEN 4:14 | Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.” |
95 | GEN 4:15 | Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. |
98 | GEN 4:18 | Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki. |
100 | GEN 4:20 | Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto. |
101 | GEN 4:21 | Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. |
103 | GEN 4:23 | Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. |
130 | GEN 5:24 | Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga. |
141 | GEN 6:3 | Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” |
152 | GEN 6:14 | Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. |
154 | GEN 6:16 | Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba. |
208 | GEN 9:2 | Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire. |
212 | GEN 9:6 | “Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. |
229 | GEN 9:23 | Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo. |
233 | GEN 9:27 | Mulungu akulitse dziko la Yafeti; Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu, ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.” |
244 | GEN 10:9 | Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” |
250 | GEN 10:15 | Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; |
251 | GEN 10:16 | Ayebusi, Aamori, Agirigasi; |
301 | GEN 12:2 | “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri. |
302 | GEN 12:3 | Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.” |
321 | GEN 13:2 | Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide. |
328 | GEN 13:9 | Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.” |
371 | GEN 15:10 | Abramu anabweretsadi zonsezi nadula chilichonse pakati nʼkuzindandalika, chidutswa chilichonse kuyangʼanana ndi chinzake; koma njiwa ndi nkhunda sanazidule pakati. |
383 | GEN 16:1 | Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; |
394 | GEN 16:12 | Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.” |
403 | GEN 17:5 | Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. |
413 | GEN 17:15 | Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. |
414 | GEN 17:16 | Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.” |
423 | GEN 17:25 | ndipo mwana wake Ismaeli anali ndi zaka khumi ndi zitatu; |
511 | GEN 20:15 | Tsono Abimeleki anati kwa Abrahamu, “Dziko langa ndi limene ukulionali; ukhale paliponse pamene ufuna.” |
512 | GEN 20:16 | Ndipo kwa Sara, iye anati, “Ndikumupatsa mlongo wakoyu makilogalamu khumi ndi awiri a siliva kutsimikiza kuti iwe ndi wosalakwa pamaso pa onse amene ali ndi iwe; ulibedi mlandu.” |
531 | GEN 21:17 | Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. |
587 | GEN 23:15 | “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.” |
635 | GEN 24:43 | taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’ |
641 | GEN 24:49 | Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.” |
652 | GEN 24:60 | Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti, “Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale mayi wa anthu miyandamiyanda; ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo.” |
672 | GEN 25:13 | Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, |
674 | GEN 25:15 | Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; |
682 | GEN 25:23 | Yehova anati kwa iye, “Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana, ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana; fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake, ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.” |
684 | GEN 25:25 | Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. |
685 | GEN 25:26 | Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa. |
695 | GEN 26:2 | Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo. |
721 | GEN 26:28 | Iwo anayankha, “Tsopano tadziwa kuti Yehova anali ndi iwe; ndiye taganiza kuti inu ndi ife tichite lumbiro. Ife tichite pangano ndi inu |
735 | GEN 27:7 | ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ |
741 | GEN 27:13 | Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.” |
751 | GEN 27:23 | Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa. |
769 | GEN 27:41 | Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.” |
782 | GEN 28:8 | Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani; |
794 | GEN 28:20 | Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; |
812 | GEN 29:16 | Tsono Labani anali ndi ana aakazi awiri; dzina la wamkulu linali Leya, ndipo dzina la wamngʼono linali Rakele. |
823 | GEN 29:27 | Yamba watsiriza sabata ya chikondwerero cha ukwati wa Leya; kenaka ndidzakupatsanso Rakele. Koma udzayenera kundigwirira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri.” |
882 | GEN 31:8 | Pamene abambo anu anati, ‘Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, ‘Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi. |
903 | GEN 31:29 | Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, ‘Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’ |
973 | GEN 33:12 | Ndipo Esau anati, “Tiyeni tizipita; nditsagana nanu.” |
1022 | GEN 35:10 | Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli. |
1023 | GEN 35:11 | Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu. |
1043 | GEN 36:2 | Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi |
1045 | GEN 36:4 | Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; |
1240 | GEN 41:44 | Kenaka Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndine Farao; tsono iwe ukapanda kulamula, palibe amene akhoza kuchita chilichonse ngakhale kuyenda kumene mʼdziko lonse la Igupto.” |
1291 | GEN 42:38 | Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.” |
1324 | GEN 43:33 | Abale aja anawakhazika patsogolo pa Yosefe. Iwo anawakhazika monga mwa mabadwidwe awo kuyambira woyamba kubadwa mpaka wotsirizira; ndipo ankangoyangʼanitsitsana modabwa. |
1419 | GEN 46:32 | Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’ |
1476 | GEN 49:2 | “Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo; mverani abambo anu Israeli. |
1477 | GEN 49:3 | “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu. |
1482 | GEN 49:8 | “Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda; dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako; abale ako adzakugwadira iwe. |
1483 | GEN 49:9 | Yuda ali ngati mwana wa mkango; umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga. Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi, ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa? |
1485 | GEN 49:11 | Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa, ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino. Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo; ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi. |
1487 | GEN 49:13 | “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja; adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi; malire ake adzafika ku Sidoni. |
1497 | GEN 49:23 | Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza; anamuthamangitsa ndi mauta awo. |
1499 | GEN 49:25 | Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri. |
1501 | GEN 49:27 | “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa; umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha, ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,” |
1535 | EXO 1:2 | Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda; |
1536 | EXO 1:3 | Isakara, Zebuloni, Benjamini; |
1537 | EXO 1:4 | Dani, Nafutali; Gadi ndi Aseri. |
1552 | EXO 1:19 | Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.” |
1592 | EXO 3:12 | Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.” |
1787 | EXO 10:9 | Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.” |
1923 | EXO 15:2 | Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza. |
1924 | EXO 15:3 | Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake. |
1926 | EXO 15:5 | Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.” |
1928 | EXO 15:7 | Ndi ulemerero wanu waukulu, munagonjetsa okutsutsani. Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu; ndipo unawapsereza ngati udzu. |
1930 | EXO 15:9 | Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.” |
1937 | EXO 15:16 | Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula. |