702 | GEN 26:9 | Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.” |
1298 | GEN 43:7 | Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, ‘Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, ‘Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?” |
9163 | 1KI 12:9 | Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ngotani? Kodi ndiwayankhe chiyani anthu amene akunena kwa ine kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anatisenzetsa’?” |