54 | GEN 2:23 | Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.” |
606 | GEN 24:14 | Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. |
15131 | PSA 75:5 | Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu. |
18581 | ISA 43:6 | Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; |
23340 | MAT 5:37 | Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo. |
23423 | MAT 8:9 | Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.” |
23924 | MAT 21:29 | “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita. |
23986 | MAT 22:45 | Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?” |
23995 | MAT 23:8 | “Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. |
23996 | MAT 23:9 | Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba. |
23997 | MAT 23:10 | Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu. |
25272 | LUK 7:8 | Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.” |
25724 | LUK 17:4 | Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.” |
26712 | JHN 13:13 | Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. |