6700 | JDG 7:4 | Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.” |
8133 | 2SA 4:10 | pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake! |
13278 | JOB 17:14 | ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’ |
18608 | ISA 44:5 | Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’ wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo; winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli. |
18631 | ISA 44:28 | Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna; iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ” |
19022 | JER 1:7 | Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. |
19087 | JER 3:16 | Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova. |
20787 | EZK 13:10 | “Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza, |
22354 | HOS 14:4 | Asiriya sangatipulumutse; ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo, sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’ kwa zimene manja athu omwe anazipanga, pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.” |
23453 | MAT 9:5 | Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ |
23706 | MAT 15:4 | Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ |
24543 | MRK 7:11 | Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), |
24800 | MRK 13:14 | “Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri. |
25261 | LUK 6:46 | “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? |
25853 | LUK 20:5 | Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’ |
25903 | LUK 21:8 | Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. |
26262 | JHN 4:37 | Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona. |
28248 | ROM 9:25 | Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,” |
30809 | REV 2:24 | Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena. |